Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 103
Matigari
“Ukhoza kundifunsa mafunso onse amene uli nawo.
Ndikufuna ndikuuzeni, mafunso ndi amene amathandiza mun-
thu kukhala wozindikira. Ndilozereni munthu amene safunsa
mafunso, kuti ndikulozereni chitsiru. Poyankha funso lako, ndi-
nakwirira zida zanga pansi pa mtengo wamkuyu. Kenako ndi-
nadzimanga ndi lamba wamtendere. Mumtima mwanga ndina-
ti: ‘Tsopano mbendera ndi ya anthu akuda. Choncho kuyambira
lero, chilungamo ndi choonadi chithetsa nkhondo zonse;
choonadi ndi chilungamo chizithetsa mikangano yonse pakati
pa ife anthu akuda. Tiyeni tilole kuti choonadi ndi chilungamo
chilamulire dziko.’”
“Koma kodi tingadziwe bwanji kuti ndinudi Matigari ma
Njiruungi? Tionetseni chizindikiro?”
“Wati chizindikiro? . . . Oh, ingodikira pang’ono, uona chi-
lungamo chikuyamba kulamulira posachedwapa . . . chifukwa
ngati sizitero . . .” Matigari anayankhula mawu amenewa ngati
munthu amene wamufunsa kuti kodi Ambuye adzabweranso
liti. “Tamvetserani . . . Sindikufunika kuchita chozizwitsa kuti
mudziwe kuti ndine ndani. Ntchito za manja anga ndi zimene
zingandichitire umboni. Ndivula lamba wamtendereyu n’kuva-
la wina wokongoletsedwa ndi zipolopolo m’malo mwa mikan-
da. Inde ndiika lamba wazipolopo m’chiunomu n’kunyamula
AK47 yanga paphewapa. Kenako ndikaima pamwamba paphiri
n’kuuza aliyense kuti: ‘Tsegulani maso kuti muone zimene ine
ndaona . . . Tsegulani mapirikaniro anu kuti mumve zimene ine
ndamva . . . Lolani kuti zofuna za anthu zichitike! Ufumu wathu
ukubwera ngati mmene anachitira abale anthu akale omwe ana-
menya nkhondo ya ufulu wawo. Nthaka ndi ya eni ake alimi
osati nthata komanso anthu ena ochokera kunja! Choncho
kuyambira lero, wolima ayenera kumakolola zimene anafesa;
womanga ayenera kumagona m’nyumba; telala ayenera
102