Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 102

Matigari “Inde, chilungamo chenicheni ndi champhamvu kuposa lu- panga. Choonadi chinakopa mlenje wina kuti asalase mdani wake yemwe ankafuna kumuboola mphafa,” wamowa uja anatero. “Koma kodi mwaiwala kuti boma lili ndi Unduna Woona Zachilungamo?” mwana wa kuyunivesite uja anawakumbutsa anzakewo. “Nduna Yoona Zachilungamo ikubwera mawa kuti idzayen- dere fakitale ija,” wogwira ntchito kufakitale uja anatero. “Ndiyetu Wofunafuna Choonadi ndi Chilungamo adzafunse ndunayo kuti choonadi ndi chilungamo chikupezeka kuti,” mnyamata wa kuyunivesite uja anatero moseka. “Ili ndiye lamu- lo loyamba: Usatchule dzina la choonadi ndi chilungamo pacha- be.” “Odi ine nditseke pakamwa panga kuti ndisapalamulenso mavuto ena!” wakuba nsima uja anatero. “Kodi awa si aphunz- itsi? Kodi posachedwapa ananena kuti amangidwa chifukwa chiyani? Anati abwera kuno chifukwa cha pakamwa. Nanga bwanji mwana wasukuluyu? Nayenso chimodzimodzi. Akulu anati ukayenda siya phazi, ukasiya pakamwa pamakutsata!” “Nanunso tiuzeni chimene chachitika kuti mupezeke kuno,” mwana wa kuyunivesite uja anatero. Onse anayamba kuseka. Munthu anali asanayankhule uja anatsukuluza kukhosi kwake. Kenako anayamba kuyankhula ndi Matigari kuti: “Kodi ndingakufunseniko funso limodzi? Mwanena kuti mwabwera kuchokera kunkhalango lero m’mawawu. Kodi zida zanu zili kuti? Kapena munali muli nazo pamene amakumangani?” 101